Pemphero Abale Wodala Gerard mu Chichewa / Nyanga


Ambuye Yesu Khristu,
Kupyolera muchaulere chanu mwandiyitana ine kuti ndikutumikireni monga mmodzi mwa otsatira uBrother wa Gerard Wodalitsika.
Ndikukuyamikani pondidalira kuti nditha kugwila ntchitoyi.
Ndikukupemphani modzichepetsa, kudzela mwa mayi athu Maria, Yohane Mbatizi, wodalitsika Gerard Tonque ndi oyera onse kuti mnjira yamoyo wauzimu wa uBrother uwonekere m’moyo mwanga ndi mnjira zamachitidwe anga zikhale zodzipereka kuntchito yanu mubanja lathu, kwa anzanga ndi ena onse ofuna chithandizo changa.
Pokhulupilira chithandizo chanu ndikufuna kuti nthawi zonse ndidziteteza chipembedzo chathu, ndikukhala okonzeka nthawi zonse kuthandiza osowa kwenikweni osauka, okwiya, aliokha, opunduka and odwala.
Ndikukupemphani kuti mundipatse mphamvu zoti ndikwanilitse kusunga malonjezowa monga mKhristu wamphamvu motsatila chipangano chanu.
Mwaulemu wa Mulungu, mwa mtendere wa dziko lapansi ndi zabwino za anthu onse.
Amen.

We thank our member Dr. Chance Chagunda for this translation into chiChewa / chiNyanja.Back to the homepage of the Brotherhood of Blessed Gérard


This page was last updated on Wednesday, 18 May 2016 12:45:24